Psalms 149

1Tamandani Yehova.

Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,
matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima.

2Israeli asangalale mwa mlengi wake;
anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo.
3Atamande dzina lake povina
ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe.
4Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake;
Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa.
5Oyera mtima asangalale mu ulemu wake
ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo.

6Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo,
ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo,
7kubwezera chilango anthu a mitundu ina,
ndi kulanga anthu a mitundu yonse,
8kumanga mafumu awo ndi zingwe,
anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo,
9kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo
Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse.

Tamandani Yehova.
Copyright information for NyaCCL